Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda May 15
“Kodi mungayankhe bwanji funso ili? [Werengani funso la pachikuto. Ndiyeno yembekezerani ayankhe.] Mfundo za m’Baibulo zimatipatsa chiyembekezo. [Werengani Mateyo 6:9, 10.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Ufumu wa Mulungu udzachite pokwaniritsa chifuniro cha Mulungu padziko lapansi.”
Galamukani! May
“Kodi mukuganiza kuti Mulungu analemberatu zochita zathu ndiponso tsogolo lathu lonse? [Yembekezerani ayankhe.] Vesi ili likusonyeza kuti Mulungu amalola anthu kusankha okha tsogolo lawo. [Werengani Deuteronomo 30:19.] Mutu uwu ukufotokoza zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi.” Asonyezeni nkhani imene yayambira pa tsamba 12.
Nsanja ya Olonda June 1
“Pafupifupi tsiku lililonse timamva nkhani za anthu amene amachita zoipa. [Tchulani zimene zangochitika kumene komanso zimene zikudziwika m’dera lanulo.] Kodi munayamba mwaganizapo kuti pali mzimu winawake woipa umene umachititsa anthu zoipazi? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno werengani Chivumbulutso 12:12.] Magaziniyi ikulongosola mmene tingadzitetezere.”
Galamukani! June
“Ndikufuna ndimve maganizo anu pa zimene lemba ili likunena. [Werengani 1 Timoteyo 6:10.] Kodi mukuvomereza kuti anthu amene amakonda kwambiri ndalama ndi chuma amagwadi m’mavuto chifukwa cha zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza mavuto amene munthu angagwemo chifukwa chofunafuna kwambiri chuma.”