Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/09 tsamba 4
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2008
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2007
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
  • Zimene Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2009
km 5/09 tsamba 4

Zomwe Munganene Pogawira Magazini

Nsanja ya Olonda May 1

Werengani Mateyo 24:3. Kenako nenani kuti: “Anthu amaona kuti funso limeneli limanena za mapeto a dziko lathu lino. Kodi mukuganiza kuti dzikoli lidzawonongedwa? [Yembekezani ayankhe.] Yankho limene Yesu anapereka limasonyeza kuti tiyenera kuyembekeza mapeto a chinachake, osati dziko lenilenili. Nkhani yomwe ili patsamba 16 ili ndi mfundo zabwino pa nkhani imeneyi.”

Galamukani! May

“Atsogoleri ena achipembedzo amanena kuti tikamasangalatsa Mulungu, adzatipatsa chuma. Komabe, n’kutheka kuti mukudziwa anthu ena abwino amene ndi osauka. Kodi mukuganiza kuti Mulungu amafuna kuti tikhale olemera? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Aheberi 13:5.] Nkhaniyi ikufotokoza mmene Mulungu amatidalitsira.” Sonyezani nkhani imene ikuyambira patsamba 12.

Nsanja ya Olonda June 1

“Masiku ano, pali mabuku ambiri a malangizo a mmene anthu angalerere ana, a zachikondi komanso ofotokoza zimene munthu angachite kuti zinthu zizimuyendera bwino. Kodi inuyo mabuku amenewa amakuthandizani? [Yembekezani ayankhe.] Anthu ambiri amanyalanyaza buku lomwe lili ndi malangizo odalirika. [Werengani 2 Timoteyo 3:16.] Magaziniyi ikufotokoza chifukwa chake tiyenera kukhulupirira Baibulo ndiponso ili ndi zitsanzo za malangizo amene amapezeka m’Baibulo.”

Galamukani! June

“Monga mukudziwira, anthu ena amaona kuti kuchotsa mimba n’koyenera pomwe ena amati sikoyenera. Kodi mukuganiza kuti Baibulo lingamuthandize munthu kusankha chochita pankhaniyi? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani 2 Timoteyo 3:16, 17.] Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limanena pankhani imeneyi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena