Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa February
“Anthu ambiri amaganiza kuti Mdyerekezi ndi amene akuchititsa zinthu zonse zoipa m’dzikoli. Komabe, iwo amadzifunsa kuti: ‘Kodi Mdyerekezi anachokera kuti? Kodi iye analengedwa ndi Mulungu?’ Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene zili apazi.” Musonyezeni nkhani imene ili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya February 1, 2013, ndipo werengani ndi kukambirana ndime yoyamba pamodzi ndi lemba lake. Mugawireni magaziniyo ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda February 1
“Tikufuna timve maganizo anu pa nkhani yokhudza munthu wina wake amene amalemekezedwa kwambiri ndi Akhristu, Ayuda ndiponso Asilamu. Munthu ameneyu ndi Mose. Kodi n’chiyani chimene chimabwera m’maganizo anu mukamva dzina lake? [Yembekezani ayankhe.] N’zochititsa chidwi kuona zimene Baibulo limanena zokhudza Mose ngakhale kuti analakwitsapo zinthu zina. [Werengani Deuteronomo 34:10-12.] Magazini iyi ikufotokoza atatu mwa makhalidwe ake abwino amene tingawatsanzire.”
Galamukani! February
“Masiku ano, anthu ambiri akusamukira kumayiko ena pothawa mavuto m’mayiko awo. Kodi mukuganiza kuti anthu amenewa nthawi zonse amapezadi zimene akufuna? [Yembekezani ayankhe.] Anthu sanayambe lero kusamukira m’mayiko ena. Taonani chitsanzo ichi cha anthu ena amene anasamuka kwawo, chomwe chikupezeka m’buku loyambirira m’Baibulo. [Werengani Genesis 46:5, 6.] Magazini iyi ikuyankha mafunso awa.” Sonyezani mwininyumba mafunso amene ali kumapeto kwa tsamba 6.