Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mwezi wa: February: Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? April ndi May: Magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!
◼ Nkhani ya onse yapadera ya pa nyengo ya Chikumbutso m’chaka cha 2011 idzakhala ya mutu wakuti “Kodi Mfundo za M’baibulo Zingatithandize pa Mavuto a Masiku Ano?”
◼ Simukufunika kudzakhala ndi misonkhano pa tsiku la Chikumbutso lomwe ndi Lamlungu pa April 17. Misonkhano yokha yomwe muyenera kudzakhala nayo ndi yokonzekera utumiki wakumunda. Mipingo imene imakhala ndi misonkhano pa tsiku limeneli, iyenera kusunthira misonkhanoyo tsiku lina mkati mwa mlungu. Ngati mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi ndipo n’zosatheka kuti musunthire misonkhanoyo tsiku lina, ndiye kuti misonkhanoyo iyenera kulephereka. Zimenezi zikachitika, mabanja ayenera kukambirana mfundo za mu Phunziro la Nsanja ya Olonda pa nthawi yawo ya Kulambira kwa Pabanja.
◼ Tikufuna kukudziwitsani kuti kuyambira tsopano woyangʼanira utumiki ndi amene adzisainira fomu yoitanitsira mabuku (S-14) osati mlembi. Mtumiki wa mabuku sayenera kusaina fomuyi mʼmalo mwa woyangʼanira utumiki. Ngati woyangʼanira utumiki palibe, mtumiki wa mabuku ayenera kupempha mkulu wina, makamaka amene ali mʼkomiti ya utumiki ya mpingo, kuti asainire fomuyo. Mkuluyo asanasainire fomuyo, aonetsetse kuti zonse zalembedwa molondola.