Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa June
“Tikucheza ndi anthu mwachidule ndipo tikukambirana nawo funso lochititsa chidwi ili. [Asonyezeni funso loyamba limene lili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya June 1.] Kodi inuyo mukuganiza bwanji?” Yembekezerani ayankhe. Kambiranani ndime zimene zili pansi pa funso limeneli komanso lemba limodzi pa malemba amene ali kumapeto kwa ndimezo. Agawireni magaziniyo, ndipo konzani zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda June 1
“Chaka chilichonse anthu pafupifupi 6 miliyoni amafa chifukwa chosuta fodya. Kodi mukuganiza kuti pali chimene anthu angachite kuti athane ndi vutoli? [Yembekezerani ayankhe.] Kuganizira mmene Mulungu amaonera nkhaniyi kwathandiza anthu ambiri kuti asiye kusuta fodya kapena kuti asayambe kusuta. Mwachitsanzo, vesi la m’Baibulo ili lathandiza anthu ena kuganizira mmene kusuta kumakhudzira ena. [Werengani 1 Akorinto 10:24.] Magaziniyi ikufotokoza kuti kuganizira zimene mawu a Mulungu amanena pa nkhani yosuta fodya, kungathandize munthu kuti asiye kusuta.”
Galamukani! June
“Masiku ano Intaneti ikupangitsa kuti anthu azipeza ocheza nawo ambirimbiri. Kodi mukuganiza kuti bwenzi labwino liyenera kukhala ndi khalidwe lotani? [Yembekezerani ayankhe.] Taonani malangizo othandiza awa ochokera m’Baibulo okhudza zimene bwenzi labwino liyenera kumachita. [Werengani Yakobo 1:19.] Magaziniyi ikufotokoza mfundo 4 zimene zingatithandize kuti tikhale bwenzi labwino.”