Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa June
Werengani Yesaya 42:8. Kenako nenani kuti: “Lembali likutiuza kuti Mulungu ali ndi dzina eti? Kodi mukuganiza kuti n’kofunika kuti tizitchula dzina la Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena.” M’patseni mwininyumbayo Nsanja ya Olonda ya June 1, ndipo kambiranani zimene zili pakamutu koyamba patsamba 16. M’siyireni magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda June 1
“Ndikufuna kumva maganizo anu pa nkhani inayake yofunika kwambiri. [Tsegulani patsamba 3 n’kusonyeza mawu amene akufotokoza mmene anthu osiyanasiyana amaonera Baibulo.] Kodi inuyo mukugwirizana ndi maganizo ati pamenepa? [Yembekezani ayankhe.] Koma kodi Baibulo ndi buku lotani? [Werengani Aroma 15:4.] Magazini iyi ikufotokoza zifukwa zisanu zimene zimasiyanitsa Baibulo ndi mabuku ena. Ikufotokozanso kufunika kwa Baibulo pa moyo wathu.”
Galamukani! June
“Chaka chilichonse, anthu ambirimbiri padziko lonse amadwala chifukwa cha chakudya chosasamalidwa bwino. Kodi mukuganiza kuti chakudya chimene timadya kudera lathu kuno chingatidwalitse? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza zinthu zinayi zimene tingachite kuti banja lathu lisamadwale chifukwa cha chakudya. Ikufotokozanso lonjezo la m’Baibulo lakuti posachedwapa aliyense adzakhala ndi chakudya chokwanira ndiponso chosayambitsa matenda.” Werengani Salimo 104:14, 15.