Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/11 tsamba 4
  • Zitsanzo za Ulaliki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zitsanzo za Ulaliki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
  • Nkhani Yofanana
  • Zomwe Munganene Pogawira Magazini
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2012
  • Zitsanzo za Ulaliki
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kodi Uchigawenga Udzatha?
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2011
km 5/11 tsamba 4

Zitsanzo za Ulaliki

Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa June

“Tonsefe tili ndi abale athu kapena anzathu amene anamwalira. Kodi mukuganiza kuti mudzawaonanso? [Yembekezani ayankhe.] Ndikufuna kukusonyeza mawu otonthoza kwambiri.” Werengani ndi kukambirana zimene zili mu Nsanja ya Olonda ya June 1, patsamba 16, pakamutu koyamba. Komanso werengani ndi kukambirana lemba limodzi limene lili pamenepo. Kenako gawirani magaziniwo, ndipo mugwirizane kuti mudzabwerenso kuti mudzakambirane yankho la funso lotsatira.

Nsanja ya Olonda June 1

“Ambirife timavutika kuti tipeze zinthu zofunika pa moyo wathu ndipo ena ndi osaukiratu. Kodi mukuganiza kuti idzafika nthawi imene sipadzakhala munthu wosauka? [Yembekezani ayankhe. Kenako werengani Salimo 9:18.] Magazini iyi ikufotokoza chimene chimachititsa umphawi. Ikufotokozanso njira yeniyeni yothetsera vutoli, imene Baibulo limanena.”

Galamukani! June

“Uchigawenga wachuluka kwambiri padzikoli. Kodi mukuganiza kuti chikuyambitsa vutoli ndi chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mawu olimbikitsa awa. [Werengani Salimo 72:7, 14.] Magazini iyi ikufotokoza zifukwa zina zimene anthu amachitira zauchigawenga. Ikufotokozanso zimene Baibulo limanena zokhudza mmene uchigawenga udzathere ndiponso kuti udzatha liti.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena