Kulemekeza Yehova Ndi Zinthu Zathu Zamtengo Wapatali
N’zosangalatsa kuona mmene mzimu wa Yehova ukulimbikitsira anthu, ngakhale ana kuthandiza pa ntchito yake. M’mbuyomu, kamnyamata kena ka zaka 9 kochokera ku mpingo wa Chirimba North, kanapita kukaona ofesi yathu ya nthambi ku Lilongwe. Iye analimbikitsidwa kwambiri chifukwa cha zimene anaona moti atabwerera kunyumba, anatumiza K1,000 yothandizira pa ntchito ya padziko lonse. Makolo ake ndi amene anam’patsa ndalamazi atakamba bwino nkhani m’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. M’malo mogula zofuna zake, anatumiza ndalamazi kuti zithandizire pa ntchito yolalikira. Zimene mwana ameneyu anachita ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa tonsefe.—2 Akor. 9:7.