Zilengezo
◼ Mabuku ogawira m’mwezi wa May: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Munthu akachita chidwi, m’patseni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. June: Gawirani buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. July ndi August: Gawirani timabuku takuti, Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Sangalalani Ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha!, Dikirani!, “Tawonani! Ndikupanga Zinthu Zonse Zatsopano, ndi kakuti, Mizimu ya Akufa—Kodi Ingakuthandizeni Kapena Kukuvulazani? Kodi Iyo Ilikodi?