Zomwe Munganene Pogawira Magazini
Nsanja ya Olonda May 15
“Kodi mukuganiza kuti mungasangalale kukhala ndi moyo zinthu zitakhala kuti zili monga mmene zafotokozedwera pa lemba louziridwa ili? [Werengani 2 Pet. 3:13. Ndiyeno yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza tanthauzo la miyamba yatsopano ndi dziko latsopano. Ikufotokozanso mmene moyo udzasinthira Mulungu akadzakwaniritsa zolinga zake zokhudza dziko lapansi.”
Galamukani! May
“Anthu ena amakhulupirira kuti ngati munthu ali wofatsa zinthu sizingamuyendere masiku ano. Mosiyana ndi maganizo amenewa, onani zimene Yesu ananena. [Werengani Mateyu 5:5, 9.] Kodi mukuvomereza zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikusonyeza kuti tingapindule m’njira zitatu, ngati titakhala anthu amtendere.” Sonyezani nkhani yomwe yayambira patsamba 28.
Nsanja ya Olonda June 1
“Nthawi inayake anthu amitundu yambiri ankalemekeza anthu okalamba, monga mmene tingaonere ndi lamulo lakalekale ili. [Werengani Levitiko 19:32.] Kodi ulemu wotere ndi wofala masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Magaziniyi ikufotokoza mmene Mulungu amasamalira anthu okalamba ndi mmene ifenso tingachitire zimenezo.”
Galamukani! June
“Uchigawenga sunayambe lero, koma masiku ano wakula kwambiri ndipo ukukhudza aliyense padziko lonse lapansi. Kodi n’chifukwa chiyani zili choncho? [Yembekezani ayankhe.] Galamukani! ino ikutchula nthawi imene uchigawenga udzatha ndiponso mmene Mulungu adzabweretsera mtendere weniweni padziko lapansi.” Werengani Mika 4:4.