Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda May 15
“Kodi munayamba mwalingalirapo ngati zinthu zimene anthu amachita padziko pano zimam’khudza Mulungu? [Yembekezani ayankhe.] Onani mmene zochita zathu zingakhudzire mtima wa Mulungu. [Ŵerengani Miyambo 27:11.] Magazini iyi ikufotokoza zitsanzo zina za anthu amene anakondweretsa mtima wa Mulungu, ndipo ikufotokoza mmene ifeyo tingachitire zomwezo.”
Galamukani! June 8
“Sayansi ya zamankhwala yapita patsogolo zedi polimbana ndi matenda, koma kodi mukuganiza kuti tidzakhala ndi dziko lopanda matenda alionse? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza kuti tsiku lina aliyense padziko lapansi adzakhala ndi thanzi langwiro pokwaniritsa lonjezo ili.” Ŵerengani Yesaya 33:24.
Nsanja ya Olonda June 1
“Anthu ena amaona kuti sikofunika kukhala m’chipembedzo chinachake pofuna kulambira Mulungu. Kodi munayamba mwaganizapo zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mbiri ya zochita za Mulungu ndi anthu m’nthaŵi zakale. Ikufotokozanso zimene kulambira Mulungu m’choonadi kumatanthauza.” Ŵerengani Yohane 4:24.
Galamukani! June 8
“Anthu ambiri masiku ano amasungulumwa. Zimenezi zimaphatikizapo kuona kuti anthu sakukufuna. Kodi simukuvomereza kuti zimenezi zingakhale zopweteka? [Yembekezani ayankhe. Ndiyeno ŵerengani Salmo 25:16.] Magazini iyi ya Galamukani! ikupereka mfundo zothandiza zogonjetsera kusungulumwa.”