Zomwe Munganene Pogaŵira Magazini
Nsanja ya Olonda June 15
“Kodi mukuganiza bwanji, kuphunzitsa ana masiku ano n’kovuta kapena ayi? [Yembekezani ayankhe.] Taonani mfundo iyi yotsimikizira kuti makolo angakwanitse kuchita zimenezo. [Ŵerengani Miyambo 22:6.] Nsanja ya Olonda iyi ili ndi malangizo abwino othandiza makolo kuti akwanitse ntchito yovuta imeneyi.”
Galamukani! July 8
“Anthu ena amaganiza kuti kukhulupirira Mulungu sikugwirizana ndi sayansi. Koma kodi mukudziŵa kuti pali akatswiri a sayansi amene amanena kuti sayansi imalimbikitsa chikhulupiriro choti kuli Mlengi? [Yembekezani ayankhe.] Galamukani! iyi ikufotokoza maumboni ena amene achititsa asayansiŵa kunena zimenezi.” Ŵerengani Aroma 1:20.
Nsanja ya Olonda July 1
“Panthaŵi za mavuto, anthu ambiri amakayika ngati Mulungu amaganiziradi anthu ndiponso ngati amaona kuvutika kwawo. Kodi inunso munakayikirapo? [Yembekezani ayankhe.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Mulungu amasonyezera kuti amatiganizira masiku ano ndi mmene waperekera njira yothetsera kuvutika konse.” Ŵerengani Yohane 3:16.
Galamukani! July 8
“Kwa anthu ambiri, unyamata ndi nthaŵi yosangalatsa komanso yovuta, kodi simukuvomereza zimenezi? [Yembekezani ayankhe.] Magazini ino ikufotokoza kusintha kumene kumachitika pa unyamata. Ikufotokozanso malangizo anzeru amene angathandize achinyamata ameneŵa kugwiritsa ntchito bwino unyamata wawo.” Ŵerengani Mlaliki 12:1.