Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Palemba la Mika 5:5 pali mawu akuti: “Tidzamutumizira abusa 7, inde atsogoleri 8 a anthu kuti akathane naye.” Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira ikuthandiza kwambiri pokwaniritsa ulosi umenewu m’Malawi muno. Tangoganizani. Makalasi 13 achitika kale pasukuluyi moti abale okwana 343 aphunzira kale pasukuluyi. Abale amenewa akutumikira m’mipingo yosiyanasiyana. Ena ndi apainiya othandiza ndipo ena ndi apainiya apadera m’mipingoyo. Kunena zoona, timathokoza kukhala ndi abale amene anapita kusukulu imeneyi m’mipingo yathu.