Ndandanda ya Mlungu wa June 11
MLUNGU WOYAMBIRA JUNE 11
Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 7 ndime 9-13 ndi bokosi patsamba 56 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Maliro 1-2 (Mph. 10)
Na. 1: Maliro 2:11-19 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Anthu “Akuwononga Dziko Lapansi” Motani?—Chiv. 11:18 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Akhristu a M’nthawi ya Atumwi Ankalemekeza Mariya Mwapadera?—rs tsa. 259 ndime 3–tsa. 260 ndime 3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Tinachita Zotani? Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mlembi. Fotokozani zimene mpingo unachita pa nyengo ya Chikumbutso. Yamikirani abale ndi alongo chifukwa cha zimene anachita pa nyengoyi. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene anasangalala nazo pamene ankagawira mapepala oitanira anthu ku Chikumbutso. Komanso afotokoze zimene anasangalala nazo pokambirana ndi anthu atsopano amene anabwera ku Chikumbutso. Abale ndi alongo amene anachita upainiya wothandiza anganene zimene zinawasangalatsa pamene ankachita upainiyawu pa nyengoyi.
Mph. 20: “Zifukwa 12 Zimene Zimatichititsa Kulalikira.” Nkhani yokambirana.
Nyimbo Na. 47 ndi Pemphero