Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa May
“Kodi mukuganiza kuti chipembedzo chimalimbikitsa chikondi ndi mtendere kapena chimalimbikitsa chidani ndi zachiwawa? [Yembekezani ayankhe.] Ndikufuna ndikusonyezeni mfundo ina yochititsa chidwi pa nkhani imeneyi.” M’patseni mwininyumbayo magazini ya Nsanja ya Olonda ya May 1 ndipo kambiranani nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi. Kenako gawirani magaziniwo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda May 1
“Anthu ambiri amaona kuti palibe vuto kuti chipembedzo ndi ndale ziziyendera limodzi. Koma ena amati chipembedzo ndi ndale siziyenera kuyendera limodzi. Inu mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Yesu anachita anthu atafuna kuti achite nawo zandale. [Werengani Yohane 6:15.] Magazini iyi ikufotokoza zimene Yesu anachita pa nkhani imeneyi ndiponso zimene Akhristu angachite kuti athandize anthu a m’dera lawo.”
Galamukani! May
“Pafupifupi munthu aliyense amene tikulankhula naye, anthu ena anamuchitirapo zinthu mopanda chilungamo. Kodi mukuganiza kuti pali njira yothetsera kupanda chilungamo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene ulosi uwu umanena za wolamulira amene adzathetse zinthu zopanda chilungamo. [Werengani Salimo 72:11-14.] Magazini iyi ikufotokoza malonjezo opezeka m’Baibulo onena za dziko lachilungamo m’tsogolomu.”