Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa April
“Akhristu ambiri amabatizidwa. Kodi mukuganiza kuti ubatizo ndi wofunikadi? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ikufotokoza mfundo zina zochititsa chidwi.” M’patseni mwininyumbayo magazini ya Nsanja ya Olonda ya April 1 ndipo kambiranani nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16 ndipo muyesetse kuwerenga ngakhale lemba limodzi. Kenako gawirani magaziniwo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda April 1
“Anthu ambiri amanena zinthu zosiyanasiyana za Yesu. Ena amaganiza kuti anali Mesiya wolonjezedwa. Ena amati anali munthu wabwino basi. Enanso amati Yesu sanakhaleko. Inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limanena kuti kudziwa zoona zenizeni za Yesu n’kofunika kwambiri. [Werengani Yohane 17:3.] Magazini iyi ili ndi mayankho a mafunso ena amene anthu ambiri amafunsa okhudza Yesu.”
Galamukani! April
“Lero tikugwira ntchito imene cholinga chake ndi kuthandiza mabanja. Kodi nanunso mukuona kuti mabanja akukumana ndi mavuto ambiri masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Taonani kumene mabanja ambiri amapezako malangizo othandiza. [Werengani Salimo 119:105.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo za m’Baibulo zimene zathandiza mabanja amene ali ndi ana owapeza kuthetsa mavuto amene amakumana nawo.”