Zochitika mu Utumiki Wakumunda
Yehova ndi Mulungu wopanda tsankho ndipo amafuna kuti “anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke” ngakhalenso akhungu. (1 Tim. 2:3, 4) Umboni wa zimenezi ndi wakuti tsopano tili ndi mipingo isanu ya Chinenero Chamanja. M’mipingo imeneyi muli ofalitsa okwana 190. Tilinso ndi timagulu tachinenero chamanja ku Kasungu, Mchinji, Mangochi, Mulanje ndi Nchalo. Apainiya apadera anatumizidwa kukathandiza ena mwa magulu amenewa kuti apite patsogolo. Mosakayikira, Yehova akudalitsa kwambiri gawo la chinenero chamanja m’Malawi muno.