Ndandanda ya Mlungu wa April 9
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 9
Nyimbo Na. 33 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 4 ndime 5-12 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Yeremiya 22-24 (Mph. 10)
Na. 1: Yeremiya 23:15-23 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Anthu Sadzatopa Ndi Moyo M’dziko Latsopano? (Mph. 5)
Na. 3: Kutsatira Mfundo za M’Baibulo Kumathandiza Kuti Banja Liziyenda Bwino—rs tsa. 388 ndime 5-8 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 15: “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Gwiritsani ntchito “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira” pokamba nkhaniyi. Kenako funsani ofalitsa kuti afotokoze zinthu zolimbikitsa zimene zinachitika chaka chatha.
Mph. 15: “Mfundo Zitatu Zimene Zingakuthandizeni Kuti Muziphunzitsa Mogwira Mtima.” Mafunso ndi mayankho. Mukamakambirana ndime 2, chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akukambirana ndi mwininyumba ndime yoyamba patsamba 3 la buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Wofalitsayo akawerenga mawu ochokera pa Yobu 10:15, afotokoze kwa mphindi imodzi kapena ziwiri kuti Yobu anali ndani. Kenako, funsani omvera chifukwa chake imeneyi si njira yabwino yophunzitsira ngakhale kuti zimene wofalitsayo wafotokoza za Yobu zinali zolondola.
Nyimbo Na. 10 ndi Pemphero