Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa November
“Anthu ambiri amafuna boma labwino. Kodi inuyo mukuganiza kuti ndi boma liti limene lingathetse mavuto amene timakumana nawo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magaziniyi ikunena.” M’patseni mwininyumbayo magazini a Nsanja ya Olonda ya November 1 ndipo kambiranani nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda November 1
“Tikufuna timve maganizo anu pa funso ili. Mukanakhala ndi mwayi wofunsa Mulungu funso limodzi, kodi ndi funso lotani limene mukanamufunsa? [Yembekezani ayankhe.] Yesu ananena kuti ndi bwino kufunafuna mayankho a mafunso amene timakhala nawo. [Werengani Mateyu 7:7.] Magazini iyi ili ndi mayankho ochokera m’Baibulo a mafunso atatu ofunikawa.” Musonyezeni mafunso amene ali m’munsi mwa tsamba 3.
Galamukani! November
“Lero tikukambirana ndi anthu nkhani yokhudza banja. Masiku ano pali mabanja ambiri amene bambo kapena mayi akulera yekha ana. Kodi mukuganiza kuti mabanja oterewa amakumana ndi mavuto ambiri kuposa mabanja amene ali ndi makolo onse? [Yembekezani ayankhe.] Makolo ambiri amapeza malangizo othandiza m’Baibulo. [Werengani 2 Timoteyo 3:16.] Magazini iyi ili ndi malangizo amene angathandize makolo amene akulera okha ana kuti zinthu ziziwayendera bwino.”