Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, gawirani buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena ngati zili zoyenera mogwirizana ndi munthuyo, gawirani timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo. November ndi December: Ofalitsa angagawire timapepala totsatirati: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa, Yehova—Kodi Iye Ndani? kapena Yesu Khristu—Kodi Iye Ndani? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. January 2013: Gawirani timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu kapena Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Pochita maulendo obwereza, gawirani buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena ngati zili zoyenera mogwirizana ndi munthuyo, gwiritsani ntchito timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha ndipo muyesetse kuyambitsa phunziro la Baibulo.