Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa January
“Timafuna titadziwa maganizo anu pa funso ili. Kodi munthu atakufunsani kuti dzina la Mulungu ndi ndani mungayankhe kuti chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena.” M’patseni mwininyumbayo Nsanja ya Olonda ya January 1 ndipo werengani ndi kukambirana nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba lomaliza. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi lokha. Kenako, konzani zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda January 1
“Anthu ambiri akhala akunena zinthu zosiyanasiyana zokhudza kutha kwa dziko. Kodi inuyo mukuganiza kuti tiyenera kuopa kutha kwa dziko? [Yembekezani ayankhe.] Lemba ili likusonyeza kuti padzakhala anthu ena amene adzapulumuke. [Werengani 1 Yohane 2:17.] Magazini iyi ikupereka mayankho a m’Baibulo a mafunso anayi amene anthu ambiri amafunsa okhudza kutha kwa dzikoli.”
Galamukani! January
“Lero tikucheza ndi mabanja n’cholinga chokambirana nawo nkhani zothandiza. Kodi mukuganiza kuti n’zofunika kuti mabanja azigwiritsa ntchito mawu awa amene ananenedwa ndi Yesu? [Werengani Machitidwe 20:35b. Kenako yembekezani ayankhe.] Kuphunzitsa ana kuti akhale osadzikonda n’kovuta masiku ano chifukwa anthu ambiri amangoganizira zofuna zawo zokha. Nkhani iyi ikufotokoza njira zina zothandiza makolo kuti aphunzitse ana awo kuti adzakhale oganizira anthu ena.”