Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa January
“Anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhani ya Mulungu. Ena amaganiza kuti Mulungu ndi wosamvetsetseka. Pamene ena amaona kuti Mulungu ndi Atate wachikondi. Kodi inuyo mumaganiza kuti Mulungu ndi wotani?” Yembekezerani ayankhe. Ndiyeno musonyezeni nkhani yomwe ili patsamba lomaliza m’magazini ya Nsanja ya Olonda ya January 1, ndipo kambiranani mfundo zomwe zili pa funso loyamba. Muwerenge lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda January 1
“Tabwera kuti tikambirane mwachidule za nkhani imene imakhudza munthu aliyense, ndipo nkhani yake ndi yonena za imfa. Kodi si zoona kuti imfa ya wachibale kapena mnzathu imakhala yowawa kwambiri? [Yembekezerani ayankhe.] Ambiri amaona kuti lemba ili ndi lotonthoza kwambiri. [Werengani Yesaya 25:8.] Magaziniyi ikufotokoza zimene Baibulo limalonjeza zoti imfa idzatha ndiponso kuti anthu amene anamwalira adzakhalanso ndi moyo.”
Galamukani! January
“Kodi ndi mavuto ati amene inuyo mukuona kuti mabanja ambiri akukumana nawo masiku ano? [Yembekezerani ayankhe.] Mwambi wa m’Baibulo uwu ukunena zimene anthu ayenera kuchita kuti banja lawo likhale lolimba. [Werengani Miyambo 24:3.] Anthu ambiri aona kuti m’Baibulo muli malangizo othandiza kwambiri mabanja. Magazini iyi ikunena za webusaiti yapadera kwambiri imene ili ndi mbali zosiyanasiyana zothandiza mabanja.”