Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa January
“Anthu ena amakhulupirira kuti Baibulo lili ndi maulosi odalirika. Ena amaona kuti lili ndi maulosi osamvetsetseka bwinobwino ndipo akhoza kumasuliridwa m’njira zosiyanasiyana. Inuyo mukuganiza bwanji?” Yembekezani ayankhe. Kenako m’patseni mwininyumbayo magazini ya Nsanja ya Olonda ya January 1 ndipo werengani ndi kukambirana nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi lokha. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda January 1
“Kodi mungavomereze zoti tikhoza kuphunzira zinthu zambiri kwa anthu amene anakhalapo kale m’mbuyomu? [Yembekezani ayankhe.] Vesi ili limatchula munthu wina wotchuka, amene ndi yekhayo amene amatchedwa kuti ‘bwenzi la Mulungu’ m’Baibulo. [Werengani Yakobo 2:23.] Magazini iyi ikufotokoza kuti n’chifukwa chiyani Mulungu ankaona Abulahamu kukhala bwenzi lake ndipo ikufotokozanso zimene tingaphunzire pa chitsanzo cha Abulahamu.”
Galamukani! January
“Ziphuphu ndiponso zinthu zina zachinyengo ndi zofala kwambiri masiku ano. Anthu ena amaganiza kuti kuchita zachinyengo pang’ono chabe n’kwabwino kuti zinthu zizikuyendera bwino. Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene mwambi wochititsa chidwi uwu umanena. [Werengani Miyambo 20:17.] Magazini iyi ikufotokoza kufunika kochita zinthu mwachilungamo.”