Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu December: Ofalitsa angagawire timapepala totsatirati: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa, Yehova—Kodi Iye Ndani? kapena Yesu Khristu—Kodi Iye Ndani? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. January ndi February 2013: Gawirani timabuku totsatirati: Kodi Mulungu Amatisamaliradi?, Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu kapena Pamene Munthu Amene Mumakonda Amwalira. Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo. March 2013: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, gwiritsani ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Ngati zili zoyenerera mogwirizana ndi mwininyumbayo, gwiritsani ntchito timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha, ndipo yesetsani kuyambitsa phunziro la Baibulo.
◼ Chikumbutso cha chaka cha 2014 chidzachitika Lolemba, pa April 14.
◼ Ofalitsa ofuna kuchita upainiya wothandiza m’mwezi wa March 2013 adzakhala ndi mwayi wosankha kupereka maola 30 kapena 50 m’mwezi umenewo. Kuwonjezera pamenepa, ngati woyang’anira dera adzakhale akuchezera mpingo wanu m’mwezi wa March, onse amene adzakhale akuchita upainiya wothandiza kaya wa maola 30 kapena 50, akudziwitsidwa kuti adzakhale nawo pamsonkhano wonse umene woyang’anira dera amachititsa ndi apainiya okhazikika.
◼ Aliyense wa ife ali ndi mwayi wopeza chimwemwe chifukwa chopereka mwakufuna kwake. (2 Akor. 9:7) Pamisonkhano yadera, yapadera, yachigawo komanso yampingo, pamakhala mabokosi a zopereka zaufulu kuti anthu azitha kupereka ndalama zothandizira ntchito yathu yapadziko lonse. Dziwani kuti zopereka zonse zothandizira ntchito yapadziko lonse ya Mboni za Yehova zimasamaliridwa ndi ofesi ya nthambi ya m’dzikolo. Chifukwa cha zimenezi tikudziwitsa anthu amene amapereka zopereka pogwiritsa ntchito cheke kuti azilemba kuti ndalamazo ziperekedwe ku “Association of Jehovah’s Witnesses of Malawi.” Zikomo kwambiri chifukwa chotsatira malangizowa.