Ndandanda ya Mlungu wa January 7
MLUNGU WOYAMBIRA JANUARY 7, 2013
Nyimbo Na. 135 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 17 ndime 8-14, ndi bokosi patsamba 137 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mateyu 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Mateyu 5:21-32 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chiyani Chingachititse Kuti Mulungu Asamve Mapemphero a Anthu Ena?—rs tsa. 340 ndime 7-tsa. 341 ndime 7 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Yehova Angakhale Bwanji ‘Cholowa Chanu’?—Num. 18:20 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini mu January. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60, fotokozani chifukwa chake magaziniwo angakhale othandiza m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti anene funso lochititsa chidwi ndiponso lemba limene angawerenge pogawira magaziniwo. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira m’magazini ya Galamukani! Ngati nthawi ilipo mungachitenso zimenezi ndi nkhani ina imodzi m’magazini ya Nsanja ya Olonda kapena Galamukani! Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Nyumba ya Ufumu Yaukhondo Imalemekezetsa Yehova. Nkhani yokambidwa ndi mkulu. Yehova ndi Mulungu woyera, chotero anthu akenso ayenera kukhala aukhondo. (Eks 30:17-21; 40:30-32) Nthawi zonse tikamasamalira malo athu olambirira kuti azikhala aukhondo komanso ooneka bwino, timapereka ulemerero kwa Yehova. (1 Pet. 2:12) Fotokozani nkhani imene inachitika m’dera lanu kapena yopezeka m’zofalitsa zathu, yosonyeza mmene kaonekedwe kabwino ka Nyumba ya Ufumu kanathandizira kuti anthu a m’deralo amve choonadi. Funsani m’bale amene amayang’anira ntchito yoyeretsa komanso kukonza Nyumba ya Ufumu yanu kuti afotokoze dongosolo limene mpingo wanu wakonza kuti nyumba yanu ya Ufumu izioneka bwino. Limbikitsani abale ndi alongo onse kuti azigwira nawo ntchito yoyeretsa komanso yokonza Nyumba ya Ufumu.
Nyimbo Na. 127 ndi Pemphero