Nkhani Zatsopano Zimene Zizipezeka mu Nsanja ya Olonda
Loweruka loyambirira la mwezi uliwonse, takhala tikugwiritsa ntchito nkhani za mu Nsanja ya Olonda zakuti, “Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena” poyambitsa maphunziro a Baibulo. Kuyambira mu January, nkhanizi zilowedwa m’malo ndi nkhani zakuti, “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo,” ndipo zizikhala kuchikuto chomaliza cha magazini yogawira. Tizigwiritsa ntchito nkhani zakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo” mu utumiki mofanana ndi mmene tinkachitira ndi nkhani zakuti, “Phunzirani Zimene Mawu a Mulungu Amanena.” (km 12/10 tsamba 2) Monga mmene zinalili m’mbuyomu, Utumiki Wathu wa Ufumu uzikhala ndi chitsanzo cha ulaliki chimene tizidzagwiritsa ntchito Loweruka loyambirira la mwezi.