Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira December 31, 2012. Taika tsiku limene likusonyeza mlungu umene mfundoyo idzakambidwe n’cholinga choti muthe kufufuza pamene mukukonzekera sukulu mlungu uliwonse.
1. Kodi ulosi wa pa Yoweli 2:1-10, 28 wonena za tizilombo timene tinalowa m’dziko ukukwaniritsidwa bwanji? [Nov. 5, w07 10/1 tsa. 13 ndime 1]
2. Kodi tikuphunzira chiyani pa uthenga wa Amosi wopita kwa Aisiraeli, Ayuda komanso anthu oyandikana nawo, umene uli pa Amosi 5:4, 6 ndi 14? [Nov. 12, w07 10/1 tsa. 15 ndime 3]
3. Kodi zikuoneka kuti n’chiyani chinachititsa Aedomu kuti akhale ndi mtima wonyada, ndipo ifeyo sitikuyenera kuiwala mfundo iti? (Obad. 3, 4) [Nov. 19, w07 11/1 tsa. 14 ndime 1]
4. Kodi Yehova anasintha bwanji maganizo ake pa nkhani ya tsoka limene ananena kuti ligwera anthu a ku Nineve? (Yona 3:8, 10) [Nov. 19, w07 11/1 tsa. 15 ndime 1]
5. Malinga ndi mawu opezeka pa Yona 4:11, n’chifukwa chiyani tiyenera kulalikira uthenga wabwino mwakhama komanso mwachifundo? [Nov. 26, w07 11/1 tsa. 15 ndime 2]
6. Kodi kukwaniritsidwa kwa ulosi umene uli pa Nahumu 2:6-10 kukutilimbikitsa bwanji? [Dec. 3, w07 11/15 tsa. 9 ndime 2; w88 2/15 tsa. 28 ndime 7]
7. Kodi lemba la Hagai 1:6, likutanthauza chiyani, ndipo ifeyo tikuphunzirapo chiyani? [Dec. 10, w06 4/15 tsa. 22 ndime 12-15]
8. Kodi tingagwiritsire ntchito bwanji malangizo othandiza amene ali pa Zekariya 7:10, akuti “musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu”? [Dec. 17, jd tsa. 113 ndime 6; w07 12/1 tsa. 11 ndime 3]
9. N’chifukwa chiyani mawu opezeka palemba la Zekariya 4:6, 7 ndi olimbikitsa kwa anthu amene akulambira Yehova masiku ano? [Dec. 17, w07 12/1 tsa. 11 ndime 1]
10. Malinga ndi zimene zili palemba la Malaki 3:16, n’chifukwa chiyani sitiyenera kufooka pamene tikuyesetsa kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu? [Dec. 31, w07 12/15 tsa. 29 ndime 3]