Ndandanda ya Mlungu wa December 31
MLUNGU WOYAMBIRA DECEMBER 31
Nyimbo Na. 37 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 17 ndime 1-7 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Malaki 1-4 (Mph. 10)
Kubwereza za M’sukulu ya Utumiki wa Mulungu (Mph. 20)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: “Nkhani Zatsopano Zimene Zizipezeka mu Nsanja ya Olonda.” Nkhani. Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba 8 posonyeza mmene tingagwiritsire ntchito magazini kuyambitsira phunziro la Baibulo pa Loweruka loyambirira la mwezi wa January.
Mph. 10: Kodi Tikuphunzirapo Chiyani? Nkhani yokambirana. Werengani Luka 10:38-42. Kambiranani mmene nkhani imeneyi ingatithandizire mu utumiki wathu.
Mph. 10: Mabuku Ogawira mu January ndi February. Nkhani yokambirana. Tchulani mfundo zachidule zimene zili m’bukulo kenako muchite zitsanzo ziwiri zosonyeza mmene tingagawirire bukulo.
Nyimbo Na. 134 ndi Pemphero