Alimbikitseni Kuti Aziyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira la Mwezi
Kuyambira ndi mwezi wa May 2011, ofalitsa analimbikitsidwa kuti aziyambitsa maphunziro a Baibulo Loweruka loyamba la mwezi uliwonse. Pofuna kutithandiza kuchita zimenezi, kumapeto kwa magazini iliyonse yogawira ya Nsanja ya Olonda kukumakhala nkhani ya mutu wakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo.” Choncho pa msonkhano wokonzekera utumiki wakumunda wa Loweruka loyambirira, wochititsa msonkhanowu azifotokoza mmene tingagwiritsire ntchito nkhani zimenezi poyambitsa maphunziro a Baibulo. Ayeneranso kukonza zoti pakhale chitsanzo chosonyeza zimenezi.
Akulu angasankhe kuti gulu lililonse lizikumana palokha pa tsikuli kapena kuti magulu onse azikumana pamodzi malo enaake kapena ku Nyumba ya Ufumu. Komabe, ngakhale zitakhala kuti mipingo ingapo imagwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumu imodzi pokonzekera utumiki, simuyenera kusintha tsiku loyambitsa maphunziro a Baibulo.