Tsiku Lapadera Loyambitsa Maphunziro a Baibulo
1 Kuyambira mu January, mpingo uliwonse uzisankha mlungu umodzi mwezi uliwonse, mwinamwake mlungu woyambirira, womwe cholinga chake chizikhala kuyambitsa maphunziro a Baibulo. Tsiku lake pa mlunguwo lizikhala Loweruka kapena Lamlungu, mogwirizana ndi mmene mpingowo ungasankhire. Patsikuli ngati mwininyumba angakane phunziro la Baibulo, ofalitsa angamupatse buku lakuti Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena magazini atsopano. Akulu ndi atumiki othandiza onse ayenera kukonza zoti azichita nawo ntchito imeneyi, ndiponso azithandiza ofalitsa kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
2 Komiti ya Utumiki ya Mpingo izisankha mlungu umene mpingo wawo ungakhale ndi tsiku loyambitsa maphunziro a Baibulo. Nthawi ndi nthawi ofalitsa ayenera kukumbutsidwa kuti akonzekere ndi kuyesetsa mwapadera kuti ayambitse maphunziro a Baibulo muutumiki wa kunyumba ndi nyumba ndiponso pobwerera kwa anthu amene anasonyeza chidwi.
3 Kukonzekera Kwake: Tingapeze njira zoyambitsira maphunziro a Baibulo mumphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2006 ndiponso m’buku la Kukambitsirana patsamba 12. Ena angayambitse maphunziro mwakugwiritsa ntchito kapepala, monga kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? Kwa anthu amene analandira magazini, tingapeze njira yoyambitsira maphunziro a Baibulo mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa August 2007, patsamba 3. Akulu ndi atumiki othandiza aziikidwa pa ndandanda yochititsa misonkhano yokonzekera utumiki wa kumunda kwa mphindi 10 kapena 15. Pamsonkhano umenewu azikambirana kapena kuchita chitsanzo cha mmene angayambitsire maphunziro a Baibulo.
4 Ndi zoona kuti si onse amene adzavomera kuphunzira Baibulo kapena kupitiriza kuphunzira. Zimenezi siziyenera kutigwetsa ulesi n’kusiya kuyambitsa maphunziro a Baibulo chifukwa Yehova ndi amene amakokera anthu onga nkhosa m’gulu lake. (Yoh. 6:44) Udindo wathu si wongofesa mbewu za choonadi koma tiyeneranso kulimirira ndi kuthirira zimene zamera kale. Njira imodzi yochitira zimenezi ndi kuphunzira Baibulo ndi anthu ofuna kuphunzira za Yehova. Tikatero ndiye kuti tidzagwiritsa bwino ntchito mwayi wathu wokhala antchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.