Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 12
Kuthandiza Ophunzira Kuyambitsa ndi Kuchititsa Maphunziro a Baibulo
1 Ophunzira Baibulo athu akayamba kupita nawo mu utumiki wa kumunda, akhoza kumachita mantha akaganiza zoyambitsa ndi kuchititsa maphunziro awoawo a Baibulo. Ndiyeno kodi tingawalimbikitse bwanji kuti azichita nawo mbali yofunika kwambiri imeneyi ya utumiki mopanda mantha?—Mat. 24:14; 28:19, 20.
2 Wophunzira Baibulo akamamuyenereza kukhala wofalitsa wosabatizidwa, amakhala atayamba kale kutenga nawo mbali mu Sukulu ya Utumiki wa Mulungu. Malangizo amene amalandira osonyeza mmene angakonzekerere ndiponso mmene angakambire nkhani za ophunzira adzamuthandiza kukhala ndi luso lophunzitsa limene limafunika kwa “wantchito wopanda chifukwa cha kuchita manyazi, wolunjika nawo bwino mawu a choonadi.”—2 Tim. 2:15.
3 Aphunzitseni Kudzera M’chitsanzo Chanu: Yesu anaphunzitsa ophunzira ake powapatsa malangizo omveka bwino ndiponso powasonyeza chitsanzo chabwino. Iye anati: “Yense, mmene atakonzedwa mtima, adzafanana ndi mphunzitsi wake.” (Luka 6:40) Kutengera chitsanzo cha Yesu mwa kusonyeza chitsanzo chabwino mu utumiki wanu n’kofunika kwambiri. Wophunzira wanu akamaona chitsanzo chanu cha mu utumiki, adzatha kumvetsetsa kuti cholinga chopangira maulendo obwereza ndicho kuyambitsa maphunziro a Baibulo.
4 M’fotokozereni kuti tikapempha munthu kuti tiziphunzira naye, sikuti timachita kufunika kufotokoza mwa tsatanetsatane ndondomeko yonse yosonyeza mmene timachitira phunziro. M’malo mwake, zimakhala bwino kungom’sonyeza mwininyumbayo mmene timaphunzirira pogwiritsa ntchito ndime imodzi kapena ziwiri kuchokera m’buku limene timaphunzitsira. Mfundo zothandiza zosonyeza mmene tingachitire zimenezi mungathe kuzipeza patsamba 8 la Utumiki Wathu wa Ufumu uno ndiponso patsamba 6 la Utumiki Wathu wa Ufumu wa January 2002.
5 Ngati n’zoyenera, m’pempheni wophunzirayo kuti mupite naye limodzi kapena kuti apite ndi wofalitsa wina wodziwa bwino ku maphunziro ena a Baibulo. Akhoza kupereka nawo ndemanga pa ndime kapena pa lemba lina lofunika. Choncho, mwa kuonera, wophunzirayo adzaphunzira zambiri zokhudza mmene angachititsire maphunziro a Baibulo opita patsogolo. (Miy. 27:17; 2 Tim. 2:2) Muyamikireni, ndipo m’fotokozereni mmene angawongolerere.
6 Kuphunzitsa ophunzira kuti akhale aphunzitsi a Mawu a Mulungu kudzawathandiza kuchita ‘ntchito yabwino’ yoyambitsa ndi kuchititsa maphunziro awoawo. (2 Tim. 3:17) N’zosangalatsatu kwambiri kugwira nawo ntchito limodzi pamene tikuitanira ena mwachikondi kuti: “Iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.”—Chiv. 22:17.