Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/04 tsamba 1
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 1:

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 1:
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Nkhani Yofanana
  • Chititsani Maphunziro a Baibulo Achidule Ndiponso a Patelefoni Opita Patsogolo
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 12
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
  • Buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Ndilo Tiziphunzitsira Anthu
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2006
  • Muzithandiza Ophunzira Baibulo Anu Kuti Afike Pobatizidwa​—Gawo 1
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 7/04 tsamba 1

Kuchititsa Maphunziro a Baibulo Opita Patsogolo Gawo 1:

Kodi Phunziro la Baibulo N’chiyani?

1 Padziko lonse, anthu a Mulungu akuchititsa maphunziro a Baibulo pafupifupi 6,000,000 mwezi uliwonse. Mwa kugwiritsa ntchito njira zabwino zophunzitsira, tingathe kuthandiza ophunzira Baibulo ameneŵa kupita patsogolo mpaka kufika podzipatulira ndi kubatizidwa komanso kukhala ‘odziŵa kuphunzitsa ena.’ (2 Tim. 2:2) Kodi mukufuna kuthandiza wophunzira wanu kuti apite patsogolo motero? Kuyambira ndi nkhani ino, Utumiki Wathu wa Ufumu uzikhala ndi nkhani zimene zizifotokoza mfundo zofunika kuti tichititse maphunziro a Baibulo opita patsogolo.

2 Pamene Muyenera Kuchitira Lipoti Phunziro la Baibulo: Ngati mumakambirana za Baibulo nthaŵi zonse mwadongosolo, ngakhale mwachidule, pogwiritsa ntchito Baibulo ndi buku limene amati tiyenera kuliphunzira ndi anthu, ndiye kuti mukuchititsa phunziro la Baibulo. Limakhalanso phunziro la Baibulo ngakhale ngati phunzirolo mumalichita choimirira pakhomo la mwininyumba kapenanso ngati mumagwiritsa ntchito telefoni. Muyenera kuchitira lipoti phunzirolo ngati mwaphunzira maulendo aŵiri kuchokera pamene munam’sonyeza kachitidwe kake ndiponso ngati zikuonetsa kuti phunzirolo lidzapitirira.

3 Zofalitsa zimene timagwiritsa ntchito pa maphunziro a Baibulo ndi bulosha la Mulungu Amafunanji ndi buku la Chidziŵitso. Tikamaliza naye mabuku ameneŵa, ndipo pali umboni wakuti munthuyo akupita patsogolo, ngakhale mochedwerapo, ndiponso wayamba kuyamikira zimene akuphunzirazo, phunzirolo liyenera kupitiriza m’buku la Lambirani Mulungu. Anthu amene sanapite kusukulu mokwanira kapena amene ali ndi vuto la kuŵerenga tingaphunzire nawo mwa kugwiritsa ntchito bulosha lakuti Mungathe Kukhala Bwenzi la Mulungu!

4 Ntchito yophunzitsa Baibulo yathandiza kwambiri anthu mamiliyoni kukhala ophunzira enieni a Yesu Kristu. (Mat. 28:19, 20) Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zidzaperekedwa mu nkhani zotsatira pankhani imeneyi, mudzatha kuchititsa maphunziro a Baibulo opita patsogolo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena