Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 7/04 tsamba 2
  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
  • Timitu
  • Mlungu Woyambira July 12
  • Mlungu Woyambira July 19
  • Mlungu Woyambira July 26
  • Mlungu Woyambira August 2
Utumiki Wathu wa Ufumu—2004
km 7/04 tsamba 2

Ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki

DZIŴANI IZI: M’miyezi ikubwerayi Utumiki Wathu wa Ufumu udzakhala ndi ndandanda ya Misonkhano ya Utumiki ya mlungu uliwonse. Mipingo ingasinthe moyenera kuti ikapezeke pa Msonkhano Wachigawo wakuti “Yendani ndi Mulungu.” Ngati n’koyenera, gwiritsani ntchito mphindi 15 pa Msonkhano wa Utumiki womaliza musanapite ku msonkhano wachigawo kuti muonenso malangizo oyenera a mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu uno amene akukhudza mpingo wanuwo. M’mwezi wa October, Msonkhano wa Utumiki umodzi udzakhala wopenda mfundo zazikulu za msonkhano wachigawo. Pokonzekera kukambiranako, tonse tikalembe notsi zofunika kumsonkhano wachigawo, komanso mfundo zapadera zimene tikufuna kuzigwiritsa ntchito pamoyo wathu ndiponso mu utumiki wa kumunda. Tikatero tidzatha kulimbikitsa ena mwa kufotokoza mmene tagwiritsira ntchito mfundozo chichokereni kumsonkhano wachigawo.

Mlungu Woyambira July 12

Nyimbo Na. 108

Mph. 9: Zilengezo za pampingo. Sankhani zilengezo zina mu Utumiki Wathu wa Ufumu uno. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, sonyezani zitsanzo za mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya July 15 ndi Galamukani! ya August 8. M’chitsanzo chimodzi, wofalitsa asonyeze mmene tingagaŵire magazini kwa munthu amene akuyenda mu msewu amene satha kulankhula bwinobwino chinenero chathu. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 18: “Tikweze Dzina Lake Pamodzi.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ikambidwe ndi mlembi wa mpingo mwa kugwiritsa ntchito mafunso amene aperekedwawo. Tchulani msonkhano wachigawo umene mpingo wagaŵiridwa. Nthaŵi ya pulogalamu yaperekedwa mu mphatika ya Utumiki Wathu wa Ufumu wa April 2004. Mungaunikire mfundo zina za mu mphatikayo ngati kuli kofunikira kutero. Pomaliza, funsani mafunso aŵiri kapena atatu kuchokera m’nkhani yakuti “Chakudya Chauzimu Chapanthaŵi Yake,” imene itsatire posachedwa pompa.

Mph. 18: “Chakudya Chauzimu Chapanthaŵi Yake.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pokambirana ndime 2, pemphani mmodzi kapena aŵiri mwa omvera kuti afotokoze mwachidule za msonkhano wachigawo wosaiŵalika umene anapezekako. Pomaliza, funsani mafunso aŵiri kapena atatu kuchokera m’nkhani yakuti “Khalani Oyera m’Makhalidwe Anu Onse,” imene idzakambidwe pa Msonkhano wa Utumiki mlungu ukubwerawu.

Nyimbo Na. 16 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 19

Nyimbo Na. 83

Mph. 7: Zilengezo za pampingo. Kambani za kufunika kotsatira pulogalamu yoŵerenga Baibulo tsiku ndi tsiku, ngakhale pamene zinthu zina zasokoneza zochita zathu. Phatikizanipo ndemanga zopezeka mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 2000, tsamba 32.

Mph. 18: “Khalani Oyera m’Makhalidwe Anu Onse.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Pemphani omvera kuti afotokoze zimene aona zomwe zimasonyeza kuti kukhala ndi khalidwe labwino pamsonkhano wachigawo kumatamanda Yehova. Pomaliza, funsani mafunso aŵiri kapena atatu kuchokera m’nkhani yakuti “Onekani Bwino Ndiponso Modzilemekeza,” imene itsatire posachedwa pompa.

Mph. 20: “Onekani Bwino Ndiponso Modzilemekeza.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Gwiritsani ntchito mafunso amene aperekedwawo. Ngati nthaŵi ilipo, ŵerengani ndi kukambirana malemba osagwidwa mawu.

Nyimbo Na. 10 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira July 26

Nyimbo Na. 216

Mph. 12: Zilengezo za pampingo. Lipoti la maakaunti. Kumbutsani ofalitsa kuti apereke malipoti awo a utumiki wa kumunda a mwezi wa July. Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zimene zili patsamba 8, sonyezani zitsanzo za mmene tingagaŵire Nsanja ya Olonda ya August 1 ndi Galamukani! ya August 8. M’chitsanzo chilichonse, asonyeze njira zosiyana za mmene tingachitire ndi anthu ofuna kulepheretsa kukambirana mwa kunena kuti ‘Kodi n’chifukwa ninji anthu inu mumafika kawirikawiri?’—Onani buku la Kukambitsirana, tsamba 20. (Ngati magazini ameneŵa sanafike pampingopo, gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulaliki cha mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa mwezi watha.)

Mph. 8: Bokosi la Mafunso. Ikambidwe ndi mkulu. Werengani ndi kukambirana nkhani yonse.

Mph. 25: “Mmene Tingalalikirire M’gawo la Malonda.” Tchulani zimene zinakonzedwa kwanuko kuti muzilalikira m’gawo la malonda. M’ndime 4-5 chitani zitsanzo zachidule zosonyeza maulaliki aŵiriwo kapena ulaliki wina umene wakhala wothandiza kwanuko. Ngati nthaŵi ilipo, pemphani omvera kuti afotokoze zokumana nazo zawo zolimbikitsa zimene apeza polalikira m’gawo la malonda.

Nyimbo Na. 173 ndi pemphero lomaliza.

Mlungu Woyambira August 2

Nyimbo Na. 60

Mph. 7: Zilengezo za pampingo.

Mph. 18: “Tsanzirani Chilungamo cha Yehova.” Kambani mawu oyamba osakwana mphindi imodzi, ndiyeno kambiranani mwa mafunso ndi mayankho. Ngati nthaŵi ilipo, pemphani omvera kupereka ndemanga pa malemba osagwidwa mawu.

Mph. 20: “Kuchititsa Maphuziro a Baibulo Opita Patsogolo—Gawo 1.” Nkhani yoti ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Athandizeni kukhala ndi chidwi pankhani za m’tsogolo zimene zikubwera. Zina mwa mfundo zimene tidzakambirana m’tsogolo muno n’zokhudza mmene tingakonzekere kuchititsa phunziro, mmene tingathandizire wophunzira kukonzekera, kuchuluka kwa zimene tingaphunzitse, mmene tingagwiritsire ntchito malemba mogwira mtima, mmene tingayankhire mafunso amene wophunzira wathu angafunse, pamene tingayambe phunziro ndi pemphero, ndi mmene tingasonyezere wophunzira kuti alidziŵe gulu. Alimbikitseni onse kugwiritsa ntchito mfundo zimene zidzafotokozedwa ndiponso kuzisunga kuti adzazigwiritse ntchito kutsogolo.

Nyimbo Na. 32 ndi pemphero lomaliza.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena