Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’mwezi wa March chaka chino, m’Malawi muno tinachititsa maphunziro a Baibulo okwana 106,307. Zimenezi zikusonyeza kuti chiwerengero cha Mboni chikhoza kuwonjezeka kwambiri m’gawo la nthambi yathu. Tikukuthokozani nonsenu chifukwa cha khama lanu. Choncho tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuti tipitirize kuthirira mbewu za choonadi zimene tinabzala m’mitima ya anthu pa nyengo ya Chikumbutso.—1 Akor. 3:6.