Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa November
“Kodi mukuganiza kuti anthu amene amamvera Mulungu amakhala osangalala? [Yembekezani ayankhe.] Nkhani iyi ili ndi mfundo zothandiza kwambiri.” Kenako m’patseni mwininyumbayo magazini ya Nsanja ya Olonda ya November 1 ndipo werengani ndi kukambirana imodzi mwa nkhani zimene zili pansi pa timitu timene tili patsamba 16 ndi 17. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi. Kenako gawirani magaziniwo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda November 1
“Anthu ena amaona kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani yogonana ndi zachikale ndiponso kungokhwimitsa zinthu. Koma ena amagwirizana ndi zimene Baibulo limanena. Inuyo mukuganiza bwanji? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene mawu awa amanena za kumene kunachokera mfundo za m’Baibulo. [Werengani 2 Timoteyo 3:16.] Magazini iyi ikufotokoza mmene Baibulo limayankhira mafunso 10 amene anthu ambiri amafunsa pa nkhani yogonana. Ikufotokozanso mmene mfundo za m’Baibulo zimatithandizira.”
Galamukani! November
“Ngati titayang’ana bwinobwino zinthu za m’chilengedwechi, kodi mukuganiza kuti tinganene kuti kuli Mlengi kapena zinthuzi zinangokhalapo zokha? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene munthu wina amene analemba nawo Baibulo ananena ataona zinthu za m’chilengedwechi. [Werengani Aroma 1:20.] Magazini iyi ikufotokoza zimene akatswiri asayansi atulukira za maselo a munthu amene akutithandiza kumvetsa nkhani imeneyi.”