Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’madera amene timakhala, nthawi zonse anthu amachita chidwi ndi Nyumba zathu za Ufumu. Pomanga nyumbazi, anthu ambiri ankayamikira abale athu chifukwa chogwira ntchito mogwirizana komanso modzipereka. Izi n’zimene zinachitikanso pamene abale ankamanga Nyumba ya Ufumu ya Namphiri ku dera la C-15 ku Ntcheu. Ndife osangalala kukudziwitsani kuti pamene timafika kumapeto kwa mwezi wa May, 2011, tinali titamanga Nyumba za Ufumu zokwana 1,018 m’Malawi muno. Yehova, yemwe ndi Womanga Wamkulu, ndi amene ali woyenera kutamandidwa chifukwa cha zimenezi.—Sal. 127:1.