Ndandanda ya Mlungu wa November 14
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 14
Nyimbo Na. 6 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cf mutu 15 ndime 17-20 ndi bokosi patsamba 160 (Mph. 25)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Mlaliki 1-6 (Mph. 10)
Na. 1: Mlaliki 6:1-12 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Kuwonjezeka kwa Kusamvera Malamulo Kukusonyeza Chiyani?—rs tsa. 264 ndime 2 ndi 3 (Mph. 5)
Na. 3: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amatsatira Malangizo a pa Aroma 12:19? (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: Kodi Mumasangalala Ndi “Mwayi Wopereka Nawo Mphatso Zachifundo”? Nkhani yokambidwa ndi mkulu yochokera mu Nsanja ya Olonda ya November 15, 2011, tsamba 22-23.
Mph. 15: “Tizichita Maulendo Obwereza kwa Anthu Amene Anasonyeza Chidwi.” Mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime yachitatu, chitani chitsanzo chosonyeza wofalitsa akulankhula yekha pokonzekera ulendo wobwereza. Iye akuonanso zimene analemba zokhudza munthuyo ndipo akuganizira zimene akayankhe pa funso limene anafunsa ndiponso zimene angachite kuti akayambitse phunziro pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani. Kambiranani mwachidule mfundo zopezeka patsamba 85 ndime 3 m’buku la Gulu, za mmene timachitira ulendo wobwereza.
Nyimbo Na. 44 ndi Pemphero