Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa November
“Tikukambirana ndi anthu funso ili. [Werengani funso loyamba lomwe lili patsamba lomaliza la Nsanja ya Olonda ya November 1.] Kodi inuyo mukuganiza bwanji? [Kambiranani mfundo zomwe zili pansi pa funso loyamba. Werengani lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo.] Ndidzabweranso kuti tidzakambirane funso lotsatirali kuti tidzadziwe chifukwa chake Yesu ankaukitsa anthu.”
Nsanja ya Olonda November 1
“Kodi munayamba mwadzifunsapo kuti n’chifukwa chiyani padzikoli pakuchitika zinthu zambiri zoipa? [Yembekezerani ayankhe.] Yankho la funsoli likupezeka palemba la Chivumbulutso 12:9. [Werengani.] Komabe, vesi 12 limasonyeza kuti posachedwapa Satana sazidzasocheretsanso anthu. [Werengani Chivumbulutso 12:12.] Nkhani iyi, ya mutu wakuti, ‘Kodi Satana Tizimuopa?’ ikufotokoza zimene tingachite kuti Satana asamatisocheretse. Yafotokozanso zomwe zidzachitikire Satan posachedwapa. Kodi mungakonde kukawerenga magaziniyi?”
Galamukani! November
“Munthu aliyense amafuna kukhala wosangalala koma anthu ambiri sakusangalala masiku ano. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chingathandize kuti munthu azikhala wosangalala? [Yembekezerani ayankhe.] Anthu ambiri amaona kuti mfundo za m’Baibulo zimawathandiza kukhala osangalala. Mwachitsanzo, taonani mfundo iyi. [Werengani Aheberi 13:5.] Magaziniyi ikufotokoza mfundo 4 za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kukhala wosangalala.”