Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa April
“Tikulimbikitsa anzathu kuti aziwerenga Baibulo. Koma anthu ambiri amaganiza kuti Baibulo ndi lovuta kulimvetsa. Kodi inunso mumaganiza choncho? [Yembekezani ayankhe.] Onani zimene limanena.” Musonyezeni kumbuyo kwa Nsanja ya Olonda ya April 1, ndipo kambiranani mfundo zimene zili pa funso loyamba. Muwerenge lemba limodzi mwa malemba amene ali pamenepo. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zodzabweranso kuti mudzakambirane funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda April 1
“Munthu aliyense amene timakambirana naye ali ndi mavuto. Zimenezi zimapangitsa anthu ena kudabwa ngati moyo wathu uli ndi phindu lililonse. Kodi mukuganiza kuti n’chiyani chimapangitsa kuti anthu asamasangalale masiku ano? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limalonjeza kuti posachedwapa Mulungu adzathetsa mavuto onse amene timakumana nawo masiku ano. [Werengani Chivumbulutso 21:4.] Magazini awa akufotokoza moyo wosangalatsa womwe tikuyembekezera m’tsogolo komanso mmene tingakhalire osangalala ngakhale masiku ano.”
Galamukani! April
“Nkhanza za m’banja sizinasiye malo, zikupezeka paliponse. Anthu ena amanena kuti chikhalidwe cha munthu, kubanja kumene anachokera komanso masewera olimbikitsa chiwawa ndi zomwe zimachititsa kuti anthu azichita nkhanza m’banja. Kodi inu mukuganiza kuti chifukwa chachikulu chimene chimachititsa kuti anthu azichitirana nkhanza m’banja n’chiyani? [Yembekezani ayankhe.] Baibulo limasonyeza mmene mwamuna ndi mkazi wake ayenera kukhalira m’banja. [Werengani Aefeso 5:33.] Magazini awa akufotokoza mmene mabanja ena athandizidwira chifukwa chogwiritsira ntchito mfundo za m’Baibulo.”