Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu March: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. April ndi May: Gawirani Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Ngati munthu ali ndi chidwi, mugawireni kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi? June: Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Yesetsani kuyambitsa maphunziro a Baibulo pa ulendo woyamba. Ofalitsa angagawirenso magazini akale ngati adakali bwino kapena angagawire kabuku kamene munthuyo angachite nako chidwi.
◼ Chaka chino Chikumbutso chichitika Lachiwiri pa March 26, 2013. Ngati mpingo wanu umachita misonkhano Lachiwiri, muyenera kusinthira tsiku lina mkati mwa mlunguwo ngati mipingo ina siigwiritsa ntchito Nyumba ya Ufumuyo. Ngati n’zosatheka kuchita Msonkhano wa Utumiki mlunguwo, wogwirizanitsa ntchito za bungwe la akulu angasankhe nkhani zimene akuona kuti n’zothandiza kwambiri ku mpingo wanu, kuti zikambidwe mlungu wina m’mwezi womwe uno. Mipingo imene idzakhala ndi woyang’anira dera iyenera kupeza tsiku lina mu mlungu womwewo limene iyenera kuchita misonkhano imene imachitika tsiku la Lachiwiri.