Ndandanda ya Mlungu wa April 1
MLUNGU WOYAMBIRA APRIL 1
Nyimbo Na. 38 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 21 ndime 1-7 ndi bokosi patsamba 166 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Luka 7-9 (Mph. 10)
Na. 1: Luka 7:18-35 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Kodi Ndi Mtundu Watsopano uti Umene Unabadwa pa Pentekosite Ndipo Cholinga Chake Chinali Chiyani?—Agal. 6:16; 1 Pet. 2:9 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Mkazi Amene Kaini Anakwatira Anachokera Kuti?—w10 9/1 tsa. 25 yafotokoza bwino mfundo ya mu rs tsa. 235 ndime 2-4 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa April. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60, fotokozani nkhani zochepa za m’magaziniwo zimene zingakhale zogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze funso lokopa chidwi limene angafunse ndiponso lemba limene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi Galamukani! Ndipo ngati nthawi ilipo mungachite zomwezo ndi nkhani imodzi ya m’magaziniwa. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Mph. 10: Zosowa za pampingo.
Mph. 10: Werengani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2013. Nkhani yokambirana. Kambiranani “Kalata Yochokera ku Bungwe Lolamulira.” Muuziretu ofalitsa ena kuti adzafotokoze zochitika zochititsa chidwi za m’buku lapachakali, zomwe n’zolimbikitsa kwambiri. Pemphani omvera kuti afotokoze ziwerengero zochititsa chidwi zomwe zikupezeka m’lipoti lapachaka la Mboni za Yehova. Pomaliza, limbikitsani anthu onse kuti amalize kuwerenga Buku Lapachaka limeneli.
Nyimbo Na. 75 ndi Pemphero