Zochitika mu Utumiki Wakumunda
M’chaka chautumiki cha 2013, abale ndi alongo 471 anaphunzira kulemba ndi kuwerenga. Tikukuthokozani abale chifukwa chothandiza anthu amenewa. Zimenezi ziwathandiza abale athuwa kuti azitha kuphunzira choonadi paokha komanso kuti aziphunzitsa mabanja awo. Ziwathandizanso kuti azilalikira mogwira mtima anthu a mitundu yonse n’cholinga choti adziwe choonadi molondola.—1 Tim. 2:4.