Ndandanda ya Mlungu wa November 10
MLUNGU WOYAMBIRA NOVEMBER 10
Nyimbo Na. 1 ndi Pemphero
Phunziro la Baibulo la Mpingo:
cl mutu 4 ndime 1-9 ndi chigawo choyamba patsamba 36 (Mph. 30)
Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Deuteronomo 19-22 (Mph. 10)
Na. 1: Deuteronomo 22:20-30 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: Mmene Uchimo Umakhudzira Ubwenzi Wathu Ndi Mulungu—rs tsa. 361 ndime 1-4 (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Baibulo Limati Chiyani pa Nkhani Yopatukana?—lv tsa. 220 ndime 2–tsa. 221 (Mph. 5)
Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 10: Funsani Woyang’anira Utumiki. Kodi ntchito yanu ndi yotani? Mukamayendera magulu a utumiki, kodi cholinga chanu chimakhala chiyani? N’chiyani chomwe anthu a m’gululo angachite kuti apindule mukamayendera gulu lawo? Wofalitsa akakufunsani zokhudza utumiki, kodi mumamuthandiza bwanji?
Mph. 20: “Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki—Muzisonyeza Chidwi Munthu Amene Mukumulalikira.” Nkhani yokambirana. Mukamaliza kukambirana nkhaniyi, chitani chitsanzo cha mbali ziwiri. Mbali yoyamba, wofalitsa agawire buku kapena kapepala komwe tikugawira mwezi uno, koma asasonyeze chidwi kwa munthuyo. Mbali yachiwiri, achitenso zomwezo koma asonyeze kuti ali ndi chidwi ndi munthuyo.
Nyimbo Na. 84 ndi Pemphero