Zitsanzo za Ulaliki
Zimene Munganene Poyambitsa Maphunziro a Baibulo Loweruka Loyambirira M’mwezi wa October
“Ndikukhulupirira kuti mungandivomereze zoti moyo ndi waufupi kwambiri. Kodi mukuganiza kuti nthawi ina anthu angadzathetse matenda ndiponso kutalikitsa moyo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene magazini iyi ikunena.” M’patseni mwininyumbayo Nsanja ya Olonda ya October 1 ndipo kambiranani nkhani imene ikupezeka pansi pa kamutu koyamba patsamba 16. Yesetsani kuwerenga ngakhale lemba limodzi. Kenako gawirani magaziniyo ndipo mukonze zoti mudzabwerenso kudzakambirana yankho la funso lotsatira.
Nsanja ya Olonda October 1
“Anthu ambiri akuda nkhawa ndi kuchuluka kwa ziphuphu m’makampani ndiponso m’boma. Kodi mukuganiza kuti pali chilichonse chimene chingachitike kuti vutoli lithe? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene lemba ili limanena zokhudza mmene Yesu adzathandizire anthu amene akuvutika chifukwa cha ziphuphu. [Werengani Salimo 72:12-14.] Magazini iyi ikufotokoza zimene zichitike posachedwapa pothetsa ziphuphu.”
Galamukani! October
“Makolo ambiri amafuna kuti ana awo akhale ophunzira bwino. Kodi mukuganiza kuti achinyamata amene akumaliza sukulu masiku ano amakhala okonzeka kuthana ndi mavuto amene angakumane nawo? [Yembekezani ayankhe.] Taonani zimene Baibulo limanena pa nkhani ya ubwino wophunzira kuti munthu akhale wozindikira komanso wanzeru. [Werengani Mlaliki 7:12.] Magazini iyi ikufotokoza mfundo zisanu zimene zingathandize ana asukulu kuti zinthu ziziwayendera bwino kusukuluko.”