Zilengezo
◼ Mabuku ogawira mu September ndi October: Gawirani magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Pochita maulendo obwereza, mungayambitse phunziro la Baibulo pogwiritsira ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena ngati n’kofunikira, gwiritsani ntchito timabuku takuti, Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha. November ndi December: Ofalitsa angagawire timapepala totsatirati: Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, Mavuto Onse a Anthu Adzatha Posachedwapa, Yehova—Kodi Iye Ndani? kapena Yesu Khristu—Kodi Iye Ndani? Ngati mwapeza anthu achidwi, asonyezeni mmene timaphunzirira Baibulo pogwiritsa ntchito buku lakuti, Baibulo Limaphunzitsa Chiyani kapena timabuku takuti Mverani Mulungu ndiponso Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha.
◼ Nkhani yapadera ya panyengo ya Chikumbutso cha 2013 idzakambidwa mlungu woyambira April 1, 2013. Mutu wa nkhaniyi udzalengezedwa m’tsogolo muno. Mipingo imene idzakhale ndi woyang’anira dera kapena msonkhano wadera mlungu umenewo idzakhale ndi nkhaniyi mlungu wotsatira. Mpingo uliwonse usadzakhale ndi nkhaniyi pasanafike pa April 1.
◼ Ngati pachitika nkhani yadzidzidzi imene mukufuna kuti ofesi ya nthambi ikuthandizeni mwamsanga, lemberani imelo ku Dipatimenti ya Utumiki pa adiresi iyi: service@mw.jw.org.