Ndandanda ya Mlungu wa October 1
MLUNGU WOYAMBIRA OCTOBER 1
Nyimbo Na. 53 ndi Pemphero
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
bt mutu 13 ndime 1-7 ndi mabokosi a patsamba 100 ndi 103 (Mph. 30)
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: Danieli 4-6 (Mph. 10)
Na. 1: Danieli 4:18-28 (Osapitirira mph. 4)
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Akhristu Oona Amapewa Kuchita Chilichonse Chogwirizana Ndi Kukhulupirira Mizimu? (Mph. 5)
Na. 3: Kodi Kale Mulungu Ankapereka Bwanji Malangizo Kwa Atumiki Ake Padziko Lapansi?—rs tsa. 140 ndime 2-3 (Mph. 5)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Yambitsani Phunziro la Baibulo Loweruka Loyambirira: Pogwiritsa ntchito chitsanzo cha ulaliki chimene chili patsamba lino, chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungayambitsire phunziro la Baibulo Loweruka loyambirira m’mwezi wa October. Limbikitsani abale ndi alongo onse kuti adzayesetse kuyambitsa nawo maphunziro a Baibulo.
Mph. 15: Kodi Tinachita Zotani Chaka Chatha? Nkhani yokambidwa ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani zimene mpingo wanu unachita mu utumiki m’chaka chautumiki chathachi, makamaka zinthu zabwino zimene unakwanitsa kuchita, ndipo uyamikireni. Konzani zoti wofalitsa mmodzi kapena awiri adzafotokoze zinthu zolimbikitsa zimene anakumana nazo. Tchulani mfundo imodzi kapena ziwiri zimene mpingo wanu uyenera kukonza chaka chimene talowachi, ndipo fotokozani zimene zingathandize mpingo wanu kuwongolera m’chaka chimenechi.
Mph. 10: Zimene Munganene Pogawira Magazini M’mwezi wa October. Nkhani yokambirana. Kwa masekondi 30 mpaka 60 fotokozani mmene magaziniwo angakhalire ogwira mtima kwa anthu a m’gawo lanu. Kenako, pogwiritsa ntchito nkhani zoyambirira za mu Nsanja ya Olonda, pemphani omvera kuti afotokoze mafunso amene angakope chidwi cha anthu ndiponso malemba amene angawerenge. Chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zoyambirira za mu Galamukani! Ngati nthawi ilipo chitaninso chimodzimodzi ndi nkhani zina za m’magaziniwa. Chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungagawirire magazini iliyonse.
Nyimbo Na. 85 ndi Pemphero