Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa—Kodi Ndidzachite Zotani Pamoyo Wanga? (Gawo 2)
Akhristu achinyamata akukumana ndi mavuto ambiri masiku ano. Pofuna kuwathandiza kuthana ndi mavutowa, kambiranani mafunso otsatirawa, omwenso angawathandize kugwiritsa ntchito moyo wawo potumikira Yehova. Mukamakambirana mafunsowa, gwiritsaninso ntchito zimene tinakambirana mlungu watha kuchokera m’buku la Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa, Buku Lachiwiri, tsamba 311 mpaka 317.
Kudzipereka ku Zinthu Zachabechabe Kapena kwa Mulungu: (1) Kodi achinyamata amalimbikitsidwa kukhala ndi zolinga zotani? (2) Kodi lemba la 1 Yohane 2:17 lingathandize bwanji achinyamata kudziwa pamene ayenera kulekezera pa nkhani ya sukulu? (3) N’chifukwa chiyani mantha sayenera kutilepheretsa kubatizidwa? (4) Tchulani zinthu zina zimene zingatithandize kuti tibatizidwe. Dziwani Zimene Muyenera Kuchita Kuti Muzisangalala ndi Utumiki: (5) N’chifukwa chiyani ena sasangalala pochita utumiki? (6) Tchulani zinthu zina zimene zingatithandize kuti tizisangalala ndi utumiki. (7) Kuwonjezera pa kuwopa kulankhula ndi anthu amene sakuwadziwa, kodi ena amaopa kwambiri chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani amaganiza choncho? (8) Kodi tingatani kuti tithetse mantha ndiponso kuti tikhale olimba mtima polankhula ndi anthu? (9) N’chifukwa chiyani tiyeneranso kuyesetsa kukhala ndi luso mu utumiki? Khomo Lotseguka Lautumiki: (10) Kodi kuchita upainiya kungatithandize bwanji kulowa pakhomo lotseguka lautumiki? (Afil. 3:16) (11) N’chifukwa chiyani anthu ena amazengereza kulowa pakhomo lautumiki limeneli? (12) Kodi ndi mfundo ziti za m’Malemba zimene zingatithandize kuti tisamade nkhawa ndi nkhani ya zachuma? (13) Kodi ena amachita zotani kuti azitha kupeza zofunikira pa moyo wawo akamachita upainiya? (14) Kodi munthu angachite chiyani ngati sangakwanitse kuyamba utumiki wa nthawi zonse?
Kufunika Kophunzira Baibulo Patokha: (15) N’chifukwa chiyani kuphunzira Baibulo patokha nthawi zonse n’kofunika? Njira Zina Zolalikirira (masiku ano timati, kulalikira m’malo opezeka anthu ambiri): (16) Kodi kuchita utumiki wosiyanasiyana kungatithandize bwanji kukhala osangalala? Utumiki wa pa Beteli: (17) Kodi munthu amene akutumikira pa Beteli amapeza madalitso otani? Sukulu Yophunzitsa Utumiki: (18) Kodi anthu amene anapita kusukulu imeneyi (imene masiku ano timati, Sukulu Yophunzitsa Baibulo ya Abale Osakwatira) apeza madalitso otani?