Utumiki wa Nthaŵi Zonse Umasangalatsa
1 Popeza ndinu wachinyamata tikukhulupirira kuti mumaganiza za tsogolo lanu. Miyambo 21:5 imatiuza kuti “zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu [“n’zaphindu,” NW].” Ngati muganiza mofatsa zimene mudzachite m’tsogolo mudzapindula. Pochita zimenezi, lingalirani zochita utumiki wa nthaŵi zonse. Chifukwa chiyani?
2 Mukafunsa achikulire ena amene anachita upainiya pa unyamata wawo kuti anaiona bwanji ntchito imeneyi, onse adzayankha kuti: “Ngati pali nthaŵi imene ndinasangalala kwambiri pamoyo wanga ndi pamene ndinkachita upainiya!” Mbale wina amene anasangalala ndi utumiki wa nthaŵi zonse kuyambira ali mnyamata, atakula anati: “Zimasangalatsa kwambiri ukakumbukira unyamata wako n’kuona kuti unatsatira langizo lanzeru lakuti: ‘Ukumbukirenso Mlengi wako masiku a unyamata wako.’” (Mlal. 12:1) Chofunika n’chakuti inu ndi makolo anu muyambe panopa kukonzekera, akuthandizeni momwe mungapezere chisangalalo chimenechi pa unyamata wanu.
3 Makolo, Limbikitsani Ana Anu Kuchita Utumiki wa Nthaŵi Zonse: Popeza Yehova ndi Atate wachikondi, amakutsogolerani njira yoti muyende. (Yes. 30:21) Potsogolera, amasonyeza chikondi kuti makolo achikristu atengerepo chitsanzo. M’malo mongowasiya ana anu kuti ayende njira imene akufuna, aphunzitseni mwanzeru njira imene afunika kuyenda kuti Yehova awadalitse. Akadzakula, zimene munawaphunzitsazo zidzawathandiza “kusiyanitsa chabwino ndi choipa.” (Aheb. 5:14) Anthu achikulire akumana ndi zambiri pamoyo ndipo amadziŵa kuti sangadalire maganizo awo; koma ayenera kudalira Yehova kuwongola mayendedwe awo. (Miy. 3:5, 6) Achinyamata afunika zimenezi kwambiri popeza sadziŵa zambiri.
4 Makolo, ana anu akamayandikira zaka za unyamata kapena ngati ali achinyamata kale, muzilankhula nawo moona mtima za ntchito zimene adzagwire. Alangizi akusukulu, aphunzitsi, ndi anzawo a m’kalasi angawalimbikitse kupeza ntchito zapamwamba za kudziko. Thandizani ana anu kusankha maphunziro a ntchito zamanja, zimene zingawathandize kupeza zinthu zofunika pamoyo wawo popanda kunyalanyaza zinthu za Ufumu. (1 Tim. 6:6-11) Nthaŵi zambiri, maphunziro a kusekondale kuphatikizapo kuphunzira ntchito ya manja ngakhale kuphunzirira pantchito pomwepo, zingathandize munthu kudzipezera bwinobwino zinthu zofunika pamoyo kwinaku akuchita utumiki wa upainiya wokhazikika.
5 Limbikitsani achinyamata kuti asafulumire kuloŵa m’banja. Nthaŵi ina akadzafuna kukwatira, adzakhala okonzeka kusamalira maudindo aakulu m’banja. Mukamalankhula za upainiya ndiponso zotumikira kugawo kumene kuli kosoŵa, muzilankhula zolimbikitsa. Mukamatero, ana anu ngakhale akali ang’onoang’ono adzafuna kugwiritsa ntchito moyo wawo kukondweretsa Yehova, kuthandiza ena, ndipo adzasangalala.
6 Achinyamata, Tsogozani Utumiki wa Nthaŵi Zonse: Achinyamata, musachite kufunsa kuti ntchito ya upainiya ndi yotani. Iyeseni mwa kuchita upainiya wothandiza kwa nthaŵi yochepa panyengo ya sukulu ngati n’kotheka ndiponso patchuti. Ndiye mudzadziŵa momwe utumiki wa upainiya umasangalatsira. Kodi mungakonze zochita upainiya wothandiza posachedwapa?
7 Ngati ndinu mbale wachinyamata m’gulu la Mulungu, ganizaninso mofatsa zoyesetsa kukhala mtumiki wotumikira. (1 Tim. 3:8-10, 12) Komanso, musankhiretu chochita mukadzakwanitsa zaka zimene amafuna, kaya kupita ku Sukulu Yophunzitsa Utumiki. Utumiki wa upainiya udzakuphunzitsani zinthu zofunika zedi, monga kuchita zinthu motsatira ndandanda, kukhala munthu wa dongosolo, kudziŵa kukhala ndi ena, ndiponso kukhala wodalirika. Zonsezi zidzakuthandizani kulandira maudindo aakulu a utumiki m’tsogolo.
8 Kuti zikuyendereni bwino mu utumiki wa nthaŵi zonse, chofunika ndi kulimbikira kuchita zinthu zokhudza utumiki wa Mulungu. Mtumwi Paulo analimbikitsa zimenezi, ndipo ananena zotsatira zake, kuti: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, . . . podziŵa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho.” (Akol. 3:23, 24) Yehova akudalitseni ndi zinthu zosangalatsa zambiri mu utumiki wa nthaŵi zonse.