Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 5/10 tsamba 3-5
  • “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
  • Nkhani Yofanana
  • Apainiya Amapereka ndi Kulandira Madalitso
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Utumiki Waupainiya—Kodi Ngoyenera Inu?
    Utumiki Wathu wa Ufumu—1998
  • Madalitso a Utumiki Waupainiya
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Ino Ndiyo Nthawi Yofunika Kulalikira!
    Utumiki Wathu wa Ufumu—2005
Onani Zambiri
Utumiki Wathu wa Ufumu—2010
km 5/10 tsamba 3-5

“Upainiya Ungakuyenereni Kwabasi!”

1. Kodi mlongo wina ananena mawu otani okhudza utumiki wake waupainiya?

1 “Palibe ntchito iliyonse imene ndikanapeza yomwe ikanakhala yosangalatsa komanso yotsitsimula mwauzimu ngati upainiya.” Ananena mawu amenewa ndi Kathe B. Palm. Kwa zaka zambirimbiri iye walalikira mwakhama m’dziko la Chile, ku South America. Poganizira mmene moyo wa anthu amene akuchita utumiki wa nthawi zonse umasangalitsira, n’kutheka kuti wina anakuuzanipo mawu akuti: “Upainiya ungakuyenereni kwabasi!”

2. N’chifukwa chiyani timakhala wosangalala kwambiri pochita zinthu zauzimu?

2 Mumakhala Wosangalala: Yesu, yemwe ndi Chitsanzo chathu, ankasangalala pochita chifuniro cha Atate wake. (Yoh. 4:34) Motero n’chifukwa chake iye anauza ophunzira ake kuti angakhale osangalaladi ngati atamachita zinthu zokhudza kulambira Yehova. Timasangalala ngati zinthu zambiri zimene timachita pamoyo wathu zili zosangalatsa Yehova. Komanso timakhala wosangalala kwambiri tikamagwiritsa ntchito nthawi, mphamvu komanso chuma chathu pothandiza ena.—Mac. 20:31, 35.

3. Kodi tingakhale osangalala motani chifukwa chowonjezera nthawi imene timathera mu utumiki?

3 Tikamathera nthawi yaitali mu utumiki m’pamenenso timakhala osangalala kwambiri chifukwa timatha kuyambitsa ndiponso kuchititsa maphunziro a Baibulo ambiri. Ngakhale m’magawo amene anthu ake amaoneka kuti alibe chidwi, tingathe kuona kuti gawolo layamba kufewa tikayamba kuzolowera utumiki ndiponso kuwonjezera luso lathu polalikira. Apainiya amaphunzitsidwa zinthu zambiri zofunika ku Sukulu ya Utumiki Waupainiya zomwe angathe kuzigwiritsa ntchito. Munthu amaloledwa kuchita nawo sukulu imeneyi akatha chaka chimodzi akuchita upainiya. (2 Tim. 2:15) Polimbikira kwambiri utumiki timabzala mbewu za choonadi zimene zingathe kudzabala zipatso mtsogolo.—Mlal. 11:6.

4. Kodi achinyamata amene atsala pang’ono kumaliza sukulu ayenera kuganizira zochita chiyani?

4 Achinyamata: Ngati mwatsala pang’ono kumaliza sukulu, kodi mwaganizirapo za tsogolo lanu? Panopo nthawi yanu yambiri imathera kuchita zinthu zakusukulu. Kodi mukamaliza sukulu nthawi imeneyo muzidzachita nayo chiyani? M’malo mogwira ntchito yolembedwa, bwanji osaganiza zochita upainiya? Pempherani kwa Yehova kuti akuthandizeni kukwaniritsa cholinga chimenechi. Upainiya umakuphunzitsani luso losiyanasiyana monga kulalikira kwa anthu osiyanasiyana, njira yabwino yothetsera mavuto, kudziletsa, ndiponso kaphunzitsidwe kabwino. Zimenezi zingakuthandizeni pa moyo wanu wonse.

5. Kodi makolo ndiponso ena onse mumpingo angatani kuti alimbikitse achinyamata kuyamba upainiya?

5 Kodi makolo mumathandiza ana anu kuti adzayambe utumiki wanthawi zonse? Mawu anu komanso chitsanzo chanu chabwino chingawathandize kuika zinthu za Ufumu pamalo oyamba m’moyo wawo. (Mat. 6:33) Ray, yemwe anayamba upainiya atangomaliza maphunziro akusekondale, anati: “Nthawi zonse mayi anga ankaona kuti munthu angakhale wosangalala kwambiri ngati akuchita upainiya.” Zinthu zimene anthu onse mumpingo amalankhula komanso kuchita zingalimbikitse anthu ena kuyamba utumiki wa upainiya. Jose, yemwe amakhala ku Spain, anati: “Aliyense mumpingo mwathu ankaona kuti ntchito yabwino kwambiri imene wachinyamata angasankhe kuchita ndi yaupainiya. Zinali zosavuta kuti ndiyambe upainiya chifukwa choti aliyense ankakonda kunena zinthu zoyamikira apainiya ndiponso ankawathandiza.”

6. Kodi tingatani ngati panopo sitilakalaka zochita upainiya?

6 Zimene Zingakufooketseni: Koma bwanji ngati mumaganiza kuti, ‘Sindinayambe ndalakalakapo zochita upainiya.’ Ngati mumaganiza choncho, pempherani kwa Yehova ndipo muuzeni kuti, ‘Sindikudziwa ngati ndingakwanitse kuchita upainiya, komabe ndikulakalaka kuchita zimene zingakukondweretseni.’ (Sal. 62:8; Miy. 23:26) Kenako fufuzani malangizo ake amene ali m’Mawu ake komanso amene gulu lake limapereka. Apainiya okhazikika ambiri anayamba ndi ‘kulawa’ upainiya pochita upainiya wothandiza ndipo ataona kuti n’zosangalatsa kwambiri anaganiza zoti ntchito yaikulu pa moyo wawo ikhale utumiki wa nthawi zonse.—Sal. 34:8.

7. Kodi tingatani ngati tikukayikira zoti tingakwanitse kulalikira kwa maola 70 mwezi uliwonse?

7 Kodi mungatani ngati mukukayikira zoti muzikwanitsa kulalikira kwa maola 70 pa mwezi? Mungachite bwino kukambirana ndi apainiya amene mumafanana nawo pa zinthu zambiri. (Miy. 15:22) Kenako lembani ndandanda zingapo ndipo musankhepo imodzi yomwe ingakuthandizeni kuti muzikwanitsa maolawo. Mungadabwe kuona kuti sizovuta kwenikweni kupeza nthawi yochita utumiki posiya kuchita zinthu zina zosafunikira kwambiri.—Aef. 5:15, 16.

8. N’chifukwa chiyani nthawi ndi nthawi tiyenera kuona mmene zinthu zilili pa moyo wathu?

8 Onaninso Mmene Zinthu Zilili pa Moyo Wanu: Zinthu zimasintha pa moyo wa munthu nthawi ndi nthawi. Choncho ndibwino kuti pakapita nthawi muziganiziranso mofatsa mmene zinthu zilili pa moyo wanu. Mwachitsanzo, kodi mwatsala pang’ono kupuma pa ntchito? Randy, yemwe anapuma pa ntchito mwamsanga, anati: “Kupuma pa ntchito mwamsanga kunandithandiza kuyamba upainiya wokhazikika limodzi ndi mkazi wanga ndiponso kunatipatsa mpata woti tisamukire kugawo lomwe kunalibe ofalitsa ambiri. Ndapeza madalitso osawerengeka chifukwa chosankha kuchita zimenezi, koma dalitso lalikulu ndi loti ndili ndi chikumbumtima chabwino.”

9. Kodi ndi mfundo iti imene anthu apabanja ayenera kuiganizira mofatsa?

9 Ataganizira bwinobwino, mabanja ena aona kuti n’zosafunikira kuti onse awiri azigwira ntchito. N’zoona kuti, kuchita zimenezi kungafune kuti banjalo lidzimane zinthu zina. Komabe madalitso amene banjalo limapeza amakhala osaneneka. John, amene mkazi wake anasiya ntchito posachedwapa kuti azichita zambiri mu utumiki ananena kuti: “Kunena zoona, ndimasangalala kwambiri kudziwa kuti mkazi wanga amathera tsiku lonse kuchita zinthu zauzimu.”

10. Kodi n’chiyani chimalimbikitsa Akhristu kuchita upainiya?

10 Zimasonyeza Chikondi ndi Chikhulupiriro: Yehova watipatsa ntchito yolalikira, imene ndi ntchito yofunika kwambiri imene aliyense wa ife angachite. Posachedwapa dongosolo lakaleli liwonongedwa ndipo okhawo amene amaitana pa dzina la Yehova ndi amene adzapulumuke. (Aroma 10:13) Kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse ndiponso kuyamikira zimene watichitira, kumatilimbikitsa kumvera lamulo la mwana wake loti tizilalikira mwakhama. (Mat. 28:19, 20; 1 Yoh. 5:3) Komanso, kukhulupirira kuti tilidi m’masiku otsiriza kumatilimbikitsa kuchita zonse zomwe tingathe mu utumiki nthawi idakalipo, m’malo mogwiritsa ntchito dzikoli mokwanira.—1 Akor. 7:29-31.

11. Kodi tiyenera kumva bwanji munthu wina akatiuza kuti upainiya ungatiyenere?

11 Sitimachita upainiya wokhazikika chifukwa choti gulu limatilimbikitsa kutero, koma timatero posonyeza kudzipereka kwa Mulungu. Choncho, wina akakuuzani kuti upainiya ungakuyenereni, dziwani kuti akukulimbikitsani kuchita zabwino. Ndipo ganizirani mofatsa komanso kupemphera kuti Yehova akuthandizeni kuyamba kugwira nawo ntchito yosangalatsa imeneyi.

[Mawu Otsindika patsamba 4]

Kodi makolo mumathandiza ana anu kuti adzayambe utumiki wanthawi zonse?

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Yehova watipatsa ntchito yolalikira, imene ndi ntchito yofunika kwambiri imene aliyense wa ife angachite.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena