Ndandanda ya Mlungu wa May 31
MLUNGU WOYAMBIRA MAY 31
□ Phunziro la Baibulo la Mpingo:
□ Sukulu ya Utumiki wa Mulungu:
Kuwerenga Baibulo: 2 Samueli 16-18
Na. 1: 2 Samueli 17:1-13
Na. 2: N’chifukwa Chiyani Yesu Amatchedwa “Mbuye wa Sabata”? (Mat.12:8)
Na. 3: Kodi Tiyenera Kulambira “Oyera Mtima” Monga Otiimira kwa Mulungu? (rs tsa. 435 ndime 9–tsa. 436 ndime 4)
□ Msonkhano wa Utumiki:
Mph. 5: Zilengezo.
Mph. 10: “Kodi Munayamba Mwasonyezapo Munthu pa Ulendo Woyamba Mmene Timachitira Phunziro la Baibulo?” Nkhani. Fotokozani maganizo amene ali mu nkhaniyo ndipo kenako chitani chitsanzo chosonyeza mmene mungawagwiritsire ntchito.
Mph. 20: “Mmene Mungaphunzitsire Ofalitsa Atsopano Kulalikira.” Nkhani ya mafunso ndi mayankho. Mukamaliza kukambirana ndime 5, chitani chitsanzo chosonyeza mkulu akulalikira ndi wofalitsa watsopano. Wofalitsa watsopanoyo akulalikira kwa munthu koma sanayese kumuwerengera munthuyo lemba lililonse. Atachoka pakhomo la munthuyo, mkuluyo akumupatsa malangizo mwanzeru komanso mwachikondi. Akumulimbikitsa watsopanoyo kuti azigwiritsa ntchito Baibulo pakhomo lililonse.